Numbers 16:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
kenaka adauza Kora pamodzi ndi gulu lake lonse kuti, “Maŵa m'maŵa, Chauta atiwonetse amene ali wakewake, ndiponso amene ali woyera mtima, ndipo adzamuuza kuti abwere pafupi naye. Munthu amene Mulungu amsankheyo, adzamufikitsa pafupi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nanena ndi Kora ndi khamu lake lonse, ndi kuti, M'mawa Yehova adzatizindikiritsa anthu ake ndi ayani, wopatulika ndani, amene adzamsendeza pafupi pa Iye; ndi iye amene anamsankha adzamsendeza pafupi pa Iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo iye anawuza Kora ndi anthu onse amene ankamutsatira kuti, “Yehova mawa mmawa adzasonyeza yemwe ndi wake ndiponso amene ndi woyera mtima. Munthuyo adzabwera pafupi ndi Iye. Munthu amene adzamusankheyo adzamusendeza pafupi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nanena ndi Kora ndi khamu lace lonse, ndi kuti, M'mawa Yehova adzatizindikiritsa anthu ace ndi ayani, wopatulika ndani, amene adzamsendeza pafupi pa iye; ndi iye amene anamsankha adzamsendeza pafupi pa iye.