Numbers 16:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
muikemo moto, ndipo muthiremo lubani maŵa pamaso pa Chauta. Munthu amene Chauta amsankheyo, ndiye woyera wake. Inu Alevi, ndinu amene mwamkitsa nazo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nimuikemo moto, muikenso chofukiza pamenepo, pamaso pa Yehova, mawa; ndipo kudzali kuti amene Yehova amsankha, wopatulika ndiye; mwakula mphamvu, inu ana a Levi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo mawa muyikemo moto ndi lubani pamaso pa Yehova. Munthu amene Yehova amusankhe ndiye amene ali woyera. Alevi inu mwawonjeza kwambiri!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nimuikemo moto, muikenso cofukiza pamenepo, pamaso pa Yehova, mawa; ndipo kudzali kuti amene Yehova amsankha, wopatulika ndiye; mwakula mphamvu, inu ana a Levi.