Numbers 16:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi simukukhutira nazo zakuti Mulungu wa Israele adakupatulani mu mpingo wa Israele, kuti mubwere pafupi ndi Mulungu kudzatumikira m'Chihema chake, ndipo kuti muime pamaso pa msonkhano ndi kuŵatumikira anthuwo?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kodi muchiyesa chinthu chaching'ono, kuti Mulungu wa Israele anakusiyanitsani ku khamu la Israele, kukusendezani pafupi pa Iye, kuchita ntchito ya Kachisi wa Yehova, ndi kuima pamaso pa khamu kuwatumikira;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi sizinakukwanireni kuti Mulungu wa Israeli anakupatulani pakati pa gulu lonse la Aisraeli ndi kukubweretsani pafupi ndi Iye, kuti muzigwira ntchito ku nyumba ya Yehova ndi kumayima pamaso pa gulu, kumatumikira?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kodi muciyesa cinthu cacing'ono, kuti Mulungu wa Israyeli anakusiyanitsani ku khamu la Israyeli, kukusendezani pafupi pa iye, kucita nchito ya kacisi wa Yehova, ndi kuima pamaso pa khamu kuwatumikira;