Numbers 17:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Chauta adauza Mose kuti, “Kabwezere ndodo ya Aroni patsogolo pa bokosi laumboni. Uisunge kuti ikhale chenjezo kwa anthu oukira aja, kuti aleke kuŵiringulako, kuti angafe.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Bweza ndodo ya Aroni kuiika chakuno cha mboni, isungike ikhale chizindikiro cha pa ana opikisana; kuti unditsirizire madandaulo ao, kuti ungafe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anawuza Mose kuti, “Bwezera ndodo ya Aaroni patsogolo pa Bokosi la Umboni, kuti chikhale chizindikiro cha kuwukira kwawo. Zimenezi zidzathetsa kudandaula kwawo kotsutsana nane, kuopa kuti angafe.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Bweza ndodo ya Aroni kulika cakuno ca mboni, isungike ikhale cizindikilo ca pa ana opikisana; kuti unelitsirizire madandaulo ao, kuti ungafe.