Numbers 17:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ulankhule ndi Aisraele kuti akupatse ndodo, fuko lililonse ndodo imodzi. Atsogoleri ao onse akupatse ndodo khumi ndi ziŵiri molingana ndi mafuko a makolo ao. Ulembe dzina la munthu aliyense pa ndodo yake,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nena ndi ana a Israele, nulandire kwa yense ndodo, banja lililonse la makolo ndodo imodzi, mtsogoleri wa mafuko ao onse monga mwa mabanja a makolo ao azipereka ndodo, zikhale khumi ndi ziwiri; nulembe dzina la yense pa ndodo yake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Yankhula ndi Aisraeli ndipo akupatse ndodo khumi ndi ziwiri, imodzi kuchokera kwa mtsogoleri wa fuko lililonse. Ulembe dzina la munthu aliyense pa ndodo yake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nena ndi ana a Israyeli, nulandire kwa yense ndodo, banja liri onse la makolo ndodo imodzi, mafuko ao onse monga mwa mabanja a makolo ao azipereka ndodo, zikhale khumi ndi ziwiri; nulembe dzina la yense pa ndodo yace.