Numbers 17:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Mose adalankhula ndi Aisraele. Ndipo atsogoleri onse adampatsa ndodozo, mtsogoleri aliyense ndodo imodzi molingana ndi mafuko a makolo ao, ndiye kuti ndodo khumi ndi ziŵiri pamodzi. Ndodo ya Aroni inali pakati pa ndodo zao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mose ananena ndi ana a Israele, ndipo akalonga ao onse anapereka, yense ndodo imodzi, monga mwa mabanja a makolo ao, ndodo khumi ndi ziwiri; ndi ndodo ya Aroni inakhala pakati pa ndodo zao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Mose anayankhula ndi Aisraeli, ndipo atsogoleri awo anapereka ndodo khumi ndi ziwiri, imodzi kuchokera kwa mtsogoleri wa fuko lililonse ndipo ndodo ya Aaroni inali pakati pa ndodo zawozo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mose ananena ndi ana a Israyeli, ndipo akalonga ao onse anapereka, yense ndodo imodzi, monga mwa mabanja a makolo ao, ndodo khumi ndi ziwiri; ndi ndodo ya Aroni inakhala pakati pa ndodo zao.