Numbers 17:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'maŵa mwake Mose adakaloŵa m'chihema chaumboni. Adangoona ndodo ya Aroni, ya fuko la Levi, itaphuka masamba nkuchitanso maluŵa, ndipo itabala zipatso zakupsa za mtundu wa matowo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali m'mawa mwake, kuti Mose analowa m'chihema cha mboni; ndipo taonani, ndodo ya Aroni, ya pa banja la Levi, inaphuka, nionetsa timaani, nichita maluwa, nipatsa akatungurume.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa tsiku lotsatira Mose analowa mu tenti ya msonkhanoyo ndipo anaona kuti ndodo ya Aaroni, yomwe inkayimira fuko la Levi, sinangophuka masamba chabe, komanso inachita maluwa nʼkubala zipatso za alimondi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali m'mawa mwace, kuti Mose analowa m'cihema ca mboni; ndipo taonani, ndodo ya Aroni, ya pa banja la Levi, inaphuka, nionetsa timaani, nicita maluwa, nipatsa akatungurume.