Numbers 18:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Chauta adauza Aroni kuti, “Iwe pamodzi ndi ana ako ndi banja la makolo ako pamodzi nawe, ndinu amene musenze zotsatira za tchimo lililonse lokhudza malo opatulika kwambiri. Ndipo iwe ndi ana ako, ndinu amene musenze zotsatira za tchimo lililonse lokhudza unsembe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anati kwa Aroni, Iwe ndi ana ako amuna ndi banja la kholo lako pamodzi ndi iwe muzisenza mphulupulu ya malo opatulika; ndipo iwe ndi ana ako amuna pamodzi ndi iwe musenze mphulupulu ya ntchito yanu ya nsembe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anawuza Aaroni kuti, “Iwe, ana ako aamuna ndi banja la abambo ako mudzasenza tchimo la malo wopatulika, koma iwe ndi ana ako aamuna okha mudzasenza tchimo lokhudza unsembe wanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anati kwa Aroni, Iwe ndi ana ako amuna ndi banja la kholo lako pamodzi ndi iwe muzisenza mphulupulu ya malo opatulika; ndipo iwe ndi ana ako amuna pamodzi ndi iwe musenze mphulupulu ya nchito yanu ya nsembe.