Numbers 18:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zinanso zanu ndi izi: zopereka zao zamphatso, ndi zopereka zoweyula za Aisraele. Zimenezi ndazipereka kwa iwe, kwa ana ako aamuna, ndi kwa ana ako aakazi amene ali ndi iwe, kuti zikhale zanu mpaka muyaya. Munthu aliyense amene ali wosaipitsidwa angathe kudyako.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zako ndi izinso: nsembe yokweza ya mphatso yao, ndi nsembe zoweyula zonse za ana a Israele; ndazipereka kwa iwe, ndi kwa ana ako amuna ndi kwa ana ako akazi pamodzi ndi iwe, likhale lemba losatha; oyera onse a m'banja lako adyeko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Izinso ndi zako: chilichonse chopatulidwa kuchokera ku mphatso zoweyula za Aisraeli ndapereka kwa iwe ndi ana ako aamuna ndi aakazi ngati gawo lako la nthawi zonse. Aliyense wa mʼnyumba mwako amene ali woyeretsedwa monga mwa mwambo angathe kudyako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zako ndi izinso: nsembe yokweza ya mphatso yao, ndi nsembe zoweyula zonse za ana a Israyeli; ndazipereka kwa iwe, ndi kwa ana ako amuna ndi kwa ana ako akazi pamodzi ndi iwe, likhale lemba losatha; oyera onse a m'banja lako adyeko.