Numbers 18:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chinthu chilichonse choyamba kubadwa, kaya ndi munthu kaya nyama, chimene amapereka kwa Chauta, chikhale chanu, Komabe mwana wamwamuna wachisamba muzimuwombola, ndiponso pakati pa nyama zosayenera kuzipereka ku nsembe, mwana wake woyamba kubadwa muzimuwombola.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zilizonse zoyambira kubadwa mwa zamoyo zonse zimene abwera nazo kwa Yehova, mwa anthu ndi mwa nyama, ndi zako; koma munthu woyamba kubadwa uzimuombola ndithu; ndi nyama yodetsa yoyamba kubadwa uziiombola.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chilichonse choyamba kubadwa kwa munthu kaya nyama, chomwe chaperekedwa kwa Yehova ndi chako. Koma uyenera kuwombola mwana aliyense wamwamuna ndi mwana aliyense woyamba wa nyama zodetsedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ziri zonse zoyambira kubadwa mwa zamoyo zonse zimene abwera nazo kwa Yehova, mwa anthu ndi mwa nyama, ndi zako; koma munthu woyamba kubadwa uzimuombola ndithu; ndi nyama yodetsa yoyamba kubadwa uziiombola.