Numbers 18:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
(Muzimuwombola akakhala wa mwezi umodzi). Uike mtengo wake woombolera kuti ukhale ndalama zisanu zasiliva, molingana ndi ndalama za ku malo opatulika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo zimene ziti zidzaomboledwa uziombole kuyambira za mwezi umodzi, monga mwa kuyesa kwako, pa ndalama za masekeli asanu, kuyesa sekeli wa malo opatulika, ndiwo magera makumi awiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene zili ndi mwezi umodzi wa kubadwa, uziwombole pa mtengo wowombolera wa ndalama zisanu zasiliva, monga mwa ndalama za ku malo wopatulika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo zimene ziti zidzaomboledwa uziombole kuyambira za rowezi umodzi, monga mwa kuyesa kwako, pa ndarama za masekeli asanu, kuyesa sekeli wa malo opatulika, ndiwo magera makumi awiri.