Numbers 18:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mwanawang'ombe woyamba kubadwa kapena mwanawankhosa woyamba kubadwa, kapenanso mwanawambuzi woyamba kubadwa, musaŵaombole. Amenewo ngoyera. Muwaze magazi ao pa guwa, ndipo mutenthe mafuta ao kuti akhale nsembe yotentha pa moto, yotulutsa fungo lokomera Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ng'ombe yoyamba kubadwa, kapena nkhosa yoyamba kubadwa, kapena mbuzi yoyamba kubadwa, usaziombola; ndizo zopatulika; uwaze mwazi wake pa guwa la nsembe, ndi kufukiza mafuta ao, nsembe yamoto ya fungo lokoma kwa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Koma usawombole ana oyamba kubadwa a ngʼombe, nkhosa kapena mbuzi. Iwo ndi opatulika. Uwaze magazi a nyamazi pa guwa lansembe ndi kutentha mafuta ake ngati nsembe yotentha ndi moto kuti likhale fungo lokoma kwa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ng'ombe yoyamba kubadwa, kapena nkhosa yoyamba kubadwa, kapena mbuzi yoyamba kubadwa, usaziombola; ndizo zopatulika; uwace mwazi wace pa guwa la nserobe, ndi kufukiza mafuta ao, nsembe yamoto ya pfungo lokoma kwa Yehova.