Numbers 18:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zopereka zonse zoyera zimene Aisraele amapereka kwa Chauta ndakupatsa iwe, ana ako aamuna ndi ana ako aakazi ali ndi iwe. Zimenezi zikhale zako mpaka muyaya. Chimenechi ndicho chipangano chamuyaya pamaso pa Chauta, chochita ndi iwe ndi ana ako.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nsembe zokweza zonse za zinthu zopatulika, zimene ana a Israele azikweza kwa Yehova, ndazipereka kwa iwe, ndi kwa ana ako amuna ndi kwa ana ako akazi pamodzi ndi iwe, likhale lemba losatha; ndilo pangano lamchere losatha, pamaso pa Yehova, kwa iwe ndi mbeu zako pamodzi ndi iwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zonse zimene mwazichotsa ku zopereka zoyera zomwe Aisraeli anapereka kwa Yehova ndazipereka kwa iwe ndi ana ako aamuna ndi aakazi ngati gawo lanu nthawi zonse. Ili ndi pangano losatha la mchere pamaso pa Yehova kwa iwe ndi ana ako.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nsembe zokweza zonse za zinthu zopatulika, zimene ana a Israyeli azikweza kwa Yehova, ndazipereka kwa iwe, ndi kwa ana ako amuna ndi kwa ana ako akazi pamodzi ndi iwe, likhale lemba losatha; ndilo pangano lamcere losatha, pamaso pa Yehova, kwa iwe ndi mbeu zako pamodzi ndi iwe.