Numbers 18:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ubwere nawonso abale ako a fuko la Levi, fuko la kholo lako, kuti azigwira nawe ntchito, azikuthandiza iwe pamodzi ndi ana ako, pamene mukutumikira m'chihema chaumboni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndiponso abale ako, fuko la Alevi, fuko la kholo lako, uwayandikizitse pamodzi ndi iwe, kuti aphatikane ndi iwe, ndi kukutumikira; koma iwe ndi ana ako pamodzi ndi iwe mukhale ku khomo la chihema cha mboni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ubweretse Alevi, abale ako, kuchokera ku fuko la abambo ako kuti azikhala ndi iwe ndi kumakuthandiza pamodzi ndi ana ako amuna pamene mukutumikira mu tenti ya umboni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndiponso abale ako, pfuko la Alevi, pfuko la kholo lako, uwayandikizitse pamodzi ndi iwe, kuti aphatikane ndi iwe, ndi kukutumikira; koma iwe ndi ana ako pamodzi ndi iwe mukhale ku khomo la cihema ca mboni.