Numbers 18:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Chauta adauza Aroni kuti, “Iwe udzakhala wopanda choloŵa m'dziko mwao, ndiponso udzakhala wopanda gawo lililonse pakati pao. Ine ndine gawo lako ndi choloŵa chako pakati pa Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Ulibe cholowa m'dziko lao, ulibe gawo pakati pao; Ine ndine gawo lako ndi cholowa chako pakati pa ana a Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Yehova anati kwa Aaroni, “Iweyo sudzakhala ndi cholowa mʼdziko lawo, ndiponso sudzalandira gawo lililonse pakati pawo. Ine ndine gawo lako ndi cholowa chako pakati pa Aisraeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Ulibe colowa m'dziko lao, ulibe gawo pakati pao; Ine ndine gawo lako ndi colowa cako pakati pa ana a Israyeli.