Numbers 18:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Alevi ndiwo amene azitumikira m'chihema chamsonkhano, ndipo adzalangidwa ngati alakwa pa udindo wao. Limeneli likhale lamulo pa mibadwo yanu yonse. Aleviwo asakhale ndi chigawo pakati pa Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Alevi azichita ntchito ya chihema chokomanako, iwo ndiwo azisenza mphulupulu yao; ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu; ndipo asakhale nacho cholowa pakati pa ana a Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Alevi ndi amene azidzagwira ntchito ya ku tenti ya msonkhano ndipo adzalangidwa chilichonse chikalakwika. Ili ndi lamulo losatha kwa mibado yawo yonse. Iwowo sadzalandira cholowa pakati pa Aisraeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Alevi azicita nchito ya cihema cokomanako, iwo ndiwo azisenza mphulupulu yao; ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu; ndipo asakhale naco colowa pakati pa ana a Israyeli.