Numbers 18:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono chachikhumi chimene Aisraele amapereka kwa Chauta, ndapatsa Aleviwo kuti chikhale chigawo chao. Nchifukwa chake ndaŵauza kuti asadzakhale ndi chigawo pakati pa Aisraele.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Popeza ndapatsa Alevi limodzi la magawo khumi, la ana a Israele, limene apereka nsembe yokweza kwa Yehova, likhale cholowa chao; chifukwa chake ndanena nao, Asadzakhale nacho cholowa mwa ana a Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼmalo mwake, ndikuwapatsa Aleviwo chakhumi ngati cholowa chawo chimene Aisraeli amapereka kwa Yehova. Nʼchifukwa chake zokhudza iwo ndinati: ‘Sadzakhala ndi cholowa pakati pa Aisraeli.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Popeza ndapatsa Alevi limodzi la magawo khumi, la ana a Israyeli, limene apereka nsembe, yokweza kwa Yehova, likhale colowa cao; cifukwa cace ndanena nao, Asadzakhale naco colowa mwa ana a Israyeli.