Numbers 18:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Uŵauzenso Alevi kuti, ‘Pamene mulandira kwa Aisraele chachikhumi chimene ndakupatsani kuti chikhale chigawo chanu, muperekeko chachikhumi cha chachikhumicho kuti chikhale nsembe kwa Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Unenenso ndi Alevi, nuti nao, Pamene mulandira kwa ana a Israele, limodzi la magawo khumi limene ndakupatsani likhale cholowa chanu chochokera kwao, muziperekako nsembe yokweza ya Yehova, limodzi la magawo khumi la limodzi la magawo khumi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Yankhula ndi Alevi ndi kunena nawo kuti, ‘Pamene mulandira chakhumi kuchoka kwa Aisraeli chimene ndimakupatsani ngati cholowa chanu, muyenera kupereka chakhumi cha choperekacho kwa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Unenenso ndi Alevi, nuti nao, Pamene mulandira kwa ana a Israyeli, limodzi la magawo khumi limene ndakupatsani likhale colowa canu cocokera kwao, muziperekako nsembe yokweza ya Yehova, limodzi la magawo khumi la limodzi la magawo khumi.