Numbers 18:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake uŵauze kuti, ‘Mutaperekako zabwino kopambana zina zonse, zotsalazo muziŵerengere kuti nzanu, monga tirigu woyamba kucha amene anthu amapuntha, ndiponso mphesa zoyamba kucha zimene amapsinya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake unene nao, Pamene mukwezako zokometsetsa zake, zidzayesedwanso kwa Alevi ngati zipatso za padwale, ndi zipatso za mopondera mphesa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Nena kwa Alevi: ‘Pamene mupereka gawo labwino lopambana zonse, gawo limenelo lidzawerengedwa kwa inu ngati lochokera popunthira tirigu kapenanso kopsinyira mphesa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace unene nao, Pamene mukwezako zokometsetsa zace, zidzayesedwanso kwa Alevi ngati zipatso za padwale, ndi zipatso za mopondera mphesa,