Numbers 18:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndaŵasankha abale ako, Alevi, pakati pa Aisraele. Iwowo ndi mphatso kwa iwe, aperekedwa kwa Chauta kuti azitumikira m'chihema chamsonkhano.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Ine, taonani, ndinatenga abale anu Alevi kuwachotsa pakati pa ana a Israele; ndiwo mphatso yanu, yopatsidwa kwa Yehova, kuchita ntchito ya chihema chokomanako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine mwini ndasankha Alevi, abale ako, pakati pa Aisraeli ngati mphatso yako ndipo aperekedwa kwa Yehova kuti azigwira ntchito ku tenti ya msonkhano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Ine, taonani, ndinatenga abale anu Alevi kuwacotsa pakati pa ana a Israyeli; ndiwo mphatso yanu, yopatsidwa kwa Yehova, kucita nchito ya cihema cokomanako.