Numbers 18:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono iwe pamodzi ndi ana ako, muzitumikira pa ntchito zaunsembe, ntchito zonse zokhudza guwa, ndi pa ntchito zonse za m'malo opatulika kwambiri. Ndakupatsa unsembe ngati mphatso yako, koma munthu wina aliyense wofika pafupi, adzaphedwa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwe ndi ana ako amuna pamodzi ndi iwe muchite ntchito yanu ya nsembe, pa zonse za ku guwa la nsembe, ndi za m'kati mwa nsalu yotchinga; ndipo mutumikire; ndikupatsani ntchito yanu ya nsembe, utumiki wopatsika kwaulere; koma mlendo wakuyandikiza amuphe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma iwe wekha ndi ana ako aamuna muzitumikira ngati ansembe ndi zina zonse zokhudza pa guwa lansembe ndi za mʼkati mwa malo wopatulika kwambiri. Ndikukupatsani mphatso ya utumiki wa unsembe. Aliyense woyandikira malo wopatulika ayenera kuphedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iwe ndi ana ako amuna pamodzi ndi iwe mucite nchito yanu ya nsembe, pa zonse za ku guwa la nsembe, ndi za m'kati mwa nsaru yocinga; ndipo mutumikire; ndikupatsani nchito yanu ya nsembe, utumiki wopatsika kwaulere; koma mlendo wakuyandikiza amuphe.