Numbers 18:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adauzanso Aroni kuti, “Pa zopereka kwa Ine, ndakupatsa zotsala zimene amasunga, ndiye kuti zinthu zimene Aisraele amapatulira Ine. Ndakupatsa zimenezi kuti zikhale gawo lako ndi la ana ako, kuti zikhale zanu mpaka muyaya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Ndipo taona, Ine ndakupatsa udikiro wa nsembe zanga zokweza, ndizo zopatulika zonse za ana a Israele; chifukwa cha kudzozedwaku ndazipereka kwa iwe, ndi kwa ana ako amuna, likhale lemba losatha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Kenaka Yehova anati kwa Aaroni, ona, Ine mwini ndikukuyika kuti ukhale woyangʼanira zopereka zobwera kwa Ine; zopereka zonse zopatulika za Aisraeli zimene amapereka kwa ine ndi kuzipereka kwa iwe ndi ana ako aamuna ngati gawo lanu la nthawi zonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Ndipo taona, Ine ndakupatsa udikiro wa nsembe zanga zokweza, ndizo zopatulika zonse za ana a Israyeli; cifukwa ca kudzozedwaku ndazipereka kwa iwe, ndi kwa ana ako amuna, likhale lemba losatha.