Numbers 18:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwa zopereka zoyera kopambana zimene sadazitenthe pa guwa, zanu zikhale izi: chepereka chonse cha chakudya, nsembe zao zonse zopepesera machimo ndi nsembe zao zonse zopepesera kupalamula, zimene amapereka kwa Ine, zonsezo zikhale zoyera kwa iwe ndi kwa ana ako.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Izi ndi zako pa zinthu zopatulika kwambiri, zosafika kumoto; zopereka zao zonse, ndi nsembe zao zonse zaufa, ndi nsembe zao zonse zauchimo, ndi nsembe zao zonse zopalamula, zimene andibwezera Ine, zikhale zopatulika kwambiri za iwe ndi za ana ako amuna.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Uzilandiranso gawo la zopereka zopatulika kwambiri zomwe sizinawotchedwe pa moto. Kuchokera pa mphatso zonse zimene amabweretsa kwa Ine ngati zopatulika kwambiri, nsembe zachakudya kapena nsembe zopepesera machimo, gawo limenelo ndi lako ndi ana ako aamuna.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Izi ndi zako pa zinthu zopatulikitsa, zosafika kumoto; zopereka: zao zonse, ndi nsembe zao zonse zaufa, ndi nsembe zao zonse zaucimo, ndi nsembe zao zonse zoparamula, zimene Andibwezera Ine, zikhale zopatulikitsa za iwe ndi za ana ako amuna.