Numbers 19:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu aliyense wokhudza munthu wakufa, ndipo sadziyeretsa, munthu ameneyo akuipitsa Chihema cha Chauta, choncho adzachotsedwa m'dziko la Aisraele. Akhale woipitsidwa chifukwa sadawazidwe madzi aja oyeretsera pa zachipembedzo, ndi woipitsidwabe ameneyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Aliyense wakukhudza mtembo wa munthu aliyense wakufa, osadziyeretsa, aipsa Kachisi wa Yehova; amsadze munthuyo kwa Israele; popeza sanamwaze madzi akusiyanitsa; ndiye wodetsedwa; kudetsedwa kwake kukali pa iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aliyense amene akhudza mtembo wa munthu nʼkulephera kudziyeretsa yekha, ndiye kuti wadetsa Nyumba ya Yehova. Munthu ameneyo achotsedwe pakati pa Aisraeli. Iye ndi wodetsedwa chifukwa sanamuwaze madzi oyeretsa; kudetsedwa kwake kukhalabe pa iyeyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ali yense wakukhudza mtembo wa munthu ali yense wakufa, osadziyeretsa, aipsa kacisi wa Yehova; amsadze munthuyo kwa Israyeli; popeza sanamwaza madzi akusiyanitsa; ndiye wodetsedwa; kudetsedwa kwace kukali pa iye.