Numbers 19:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu aliyense amene akhudza munthu wophedwa ndi lupanga panja, kapena mtembo, kapena fupa la munthu wakufa, kapenanso manda, akhala woipitsidwa masiku asanu ndi aŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo aliyense wakukhudza munthu wophedwa ndi lupanga, kapena mtembo, kapena fupa la munthu, kapena manda, pathengo poyera, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Aliyense wokhudza munthu amene waphedwera kunja ndi lupanga kapena amene wafa ndi imfa ya chilengedwe, kapena aliyense wokhudza fupa la munthu kapena manda, munthu ameneyo adzakhala wodetsedwa kwa masiku asanu ndi awiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ali yense wakukhudza munthu wophedwa ndi lupanga, kapena mtembo, kapena pfupa la munthu, kapena manda, pathengo poyera, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri.