Numbers 19:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono munthu wosaipitsidwa atenge kachitsamba ka hisope ndi kukaviika m'madzi aja, ndipo awaze madziwo pa hema, pa zipangizo zake zonse, pa anthu amene anali m'menemo, ndi pa munthu amene adakhudza fupa la munthu wakufa, kapena munthu wophedwa, kapena chikulu mtembo kapena manda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi munthu woyera atenge hisope, namviike m'madzimo, ndi kuwawaza pahema ndi pa zotengera zonse, ndi pa anthu anali pomwepo, ndi pa iye wakukhudza fupa, kapena wophedwa, kapena wakufa, kapena manda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono munthu woyeretsedwa atenge hisope, amuviyike mʼmadzi ndi kuwaza tentiyo ndi zipangizo zonse, pamodzi ndi anthu anali mʼmenemo. Ayenera kuwazanso aliyense wakhudza fupa kapena, munthu wochita kuphedwa, kapena amene wafa ndi imfa ya chilengedwe kapenanso amene wakhudza manda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi munthu woyera atenge hisope, nambviike m'madzimo, ndi kuwawaza pahema ndi pa zotengera zonse, ndi pa anthu anali pomwepo, ndi pa iye wakukhudza pfupa, kapena wophedwa, kapena wakufa, kapena Manda.