Numbers 19:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu amene ali wosaipa pa zachipembedzo ndiye aole phulusa la ng'ombelo, ndipo aliike kunja kwa mahema pa malo aukhondo pa zachipembedzo. Asungire mpingo wa Aisraele phulusalo, kuti aziika m'madzi oyeretsera zonyansa pa zachipembedzo. Mwambo umenewu ndi wochotsera tchimo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo munthu woyera aole mapulusa a ng'ombe yaikaziyo, nawaike kunja kwa chigono, m'malo moyera: ndipo awasungire khamu la ana a Israele akhale a madzi akusiyanitsa; ndiwo nsembe yauchimo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Munthu amene ndi woyeretsedwa achotse phulusa la ngʼombeyo ndi kuliyika pa malo woyeretsedwa kunja kwa msasa. Aisraeli adzasunge phulusalo kuti azikaligwiritsa ntchito polithira mʼmadzi woyeretsera ndi wochotsera tchimo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo munthu woyera aole mapulusa a ng'ombe ya msotiyo, nawaike kunja kwa cigono, m'malo moyera: ndipo awasungire khamu la ana a lsrayeli akhale a madzi akusiyanitsa; ndiwo nsembe yaucimo.