Numbers 2:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chiŵerengero chathunthu cha anthu a m'zithando za Rubeni, poŵerenga magulu atatu onseŵa, ndi 151,450. Iwo akhale a gulu lachiŵiri poyenda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Owerengedwa onse a chigono cha Rubeni ndiwo zikwi makumi khumi mphambu makumi asanu ndi chimodzi kudza mazana anai mphambu makumi asanu, monga mwa makamu ao. Ndiwo azitsatana nao otsogolerawo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu onse aamuna mu msasa wa Rubeni, chiwerengero chawo monga mwa magulu awo, ndi 151,450. Iwowo azikhala achiwiri posamuka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Owerengedwa onse a cigono ca Rubeni ndiwo zikwi makumi khumi mphambu makumi asanu ndi cimodzi kudza mazana anai mphambu makumi asanu, monga mwa makamu ao. Ndiwo azitsatana nao otsogolerawo.