Numbers 2:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Pamenepo mpamene anyamule chihema chamsonkhano, chifukwa zithando za Alevi zimakhala pakati pa zithando zina. Monga momwe adamangira zithando zao, ndimo aziyendera, gulu lililonse pamalo pake motsatira mbendera yake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo khamu la Alevi azimuka nacho chihema chokomanako, pakati pa makamu; monga amamanga mahema ao, momwemo azimuka ulendo wao, munthu yense pamalo pake, monga mwa mbendera zao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono tenti ya msonkhano ndi msasa wa Alevi zidzakhala pakati pa misasayo. Iwo adzasamuka monga momwe anamangira misasa yawo, aliyense pa malo ake pamene pali mbendera yake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo khamu la Alevi azimuka naco cihema cokomanako, pakati pa makamu; monga amamanga mahema ao, momwemo azimuka ulendo wao, munthu yense pamalo pace, monga mwa mbendera zao.