Numbers 2:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Mbali yakuzambwe kuzikhala mbendera ya zithando za fuko la Efuremu, m'magulumagulu. Mtsogoleri wa fuko la Efuremulo ndi Elisama mwana wa Amihudi,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mbendera ya chigono cha Efuremu izikhala kumadzulo monga mwa makamu ao; ndipo kalonga wa ana a Efuremu ndiye Elisama mwana wa Amihudi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kumadzulo kudzakhala magulu a msasa wa Efereimu pamene pali mbendera yawo. Mtsogoleri wa Aefereimuwo ndi Elisama mwana wa Amihudi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mbendera ya cigono ca Efraimu izikhala kumadzulo monga mwa makamu ao; ndipo kalonga wa ana a Efraimu ndiye Elisama mwana wa Amihudi.