Numbers 2:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chiŵerengero chathunthu cha anthu a m'zithando za Efuremu, poŵerenga magulu atatu onseŵa, ndi 108,100. Iwo akhale a gulu lachitatu poyenda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Owerengedwa onse a chigono cha Efuremu ndiwo zikwi makumi khumi mphambu zisanu ndi zitatu kudza zana limodzi, monga mwa makamu ao. Iwo ndiwo aziyenda gulu lachitatu paulendo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu onse aamuna mu msasa wa Efereimu, chiwerengero chawo ndi 108,100 monga mwa magulu awo. Iwowo azikhala achitatu posamuka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Owerengedwa onse a cigono ca Efraimu ndiwo zikwi makumi khumi mphambu zisanu ndi zitatu kudza zana limodzi, monga mwa makamu ao. Iwo ndiwo aziyenda gulu lacitatu paulendo.