Numbers 2:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Mbali yakumpoto kuzikhala mbendera ya zithando za fuko la Dani, m'magulumagulu. Mtsogoleri wa fuko la Danilo ndi Ahiyezere mwana wa Amishadai,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mbendera ya chigono cha Dani izikhala kumpoto monga mwa makamu ao; ndi kalonga wa ana a Dani ndiye Ahiyezere mwana wa Amisadai.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kumpoto kudzakhala msasa wa magulu a Dani pamene pali mbendera yawo. Mtsogoleri wa Adani ndi Ahiyezeri mwana wa Amisadai.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mbendera ya cigono ca Dani izikhala kumpoto monga mwa makamu ao; ndi kalonga wa ana a Dani ndiye Ahiyezeri mwana wa Amisadai.