Numbers 2:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amene amange pafupi ndi fuko lake akhale a fuko la Asere, limene mtsogoleri wake ndi Pagiyele mwana wa Okarani,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwo a kumanga mahema ao poyandikizana naye ndiwo a fuko la Asere; ndi kalonga wa ana a Asere ndiye Pagiyele mwana wa Okarani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Fuko la Aseri lidzamanga pafupi ndi iwowo. Mtsogoleri wa Aaseri ndi Pagieli mwana wa Okirani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iwo akumanga mahema ao poyandikizana naye ndiwo a pfuko la Aseri; ndi kalonga wa ana a Aseri ndiye Pagiyeli mwana wa Okirani.