Numbers 2:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amene amange kuvuma, kotulukira dzuŵa, akhale a mbendera ya zithando za fuko la Yuda, m'magulumagulu. Mtsogoleri wa fuko la Yudalo ndi Nasoni, mwana wa Aminadabu,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwo akumanga mahema ao ku m'mawa kotuluka dzuwa ndiwo a mbendera ya chigono cha Yuda, monga mwa makamu ao; ndipo kalonga wa ana Yuda ndiye Nasoni mwana wa Aminadabu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kummawa, kotulukira dzuwa, magulu a msasa wa Yuda amange pamene pali mbendera yawo. Mtsogoleri wa Ayudawo ndi Naasoni mwana wa Aminadabu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iwo akumanga mahema ao ku m'mawa koturuka dzuwa ndiwo a mbendera ya cigono ca Yuda, monga mwa makamu ao; ndipo kalonga wa ana a Yuda ndiye Nahesoni mwana wa Aminadabu.