Numbers 2:32 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ameneŵa ndiwo Aisraele monga momwe adaŵaŵerengera potsata banja la makolo ao. Anthu onse a m'zithandomo anali 603,550 amene adaŵaŵerenga m'magulumagulu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Amenewo ndiwo anawerengedwa a ana a Israele monga mwa nyumba za makolo ao; owerengedwa onse a m'zigono, monga mwa makamu ao, ndiwo zikwi makumi khumi kasanu ndi kamodzi mphambu zitatu kudza mazana asanu ndi makumi asanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amenewa ndi Aisraeli monga mwa mabanja a makolo awo. Chiwerengero cha Aisraeli onse mʼmisasa chinali 603,550, mwa magulu awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Amenewo ndiwo anawerengedwa a ana a Israyeli monga mwa nyumba za makolo ao; owerengedwa onse a m'zigono, monga mwa makamu ao, ndiwo zikwi makumi khumi kasanu ndi kamodzi mphambu zitatu kudza mazana asanu ndi makumi asanu.