Numbers 20:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa mwezi woyamba, mpingo wonse wa Aisraele udafika ku chipululu cha Zini, ndipo anthuwo adakhala ku Kadesi. Miriyamu adafera kumeneko naikidwa komweko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ana a Israele, ndilo khamu lonse, analowa m'chipululu cha Zini mwezi woyamba; ndipo anthu anakhala m'Kadesi; kumeneko anafa Miriyamu, naikidwa komweko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa mwezi woyamba gulu lonse la Aisraeli linafika ku chipululu cha Zini, ndipo anakhala ku Kadesi. Miriamu anafera kumeneko ndipo anayikidwa mʼmanda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ana a Israyeli, ndilo khamu lonse, analowa m'cipululu ca Zini mwezi woyamba; ndipo anthu anakhala m'Kadesi; kumeneko anafa Miriamu, naikidwakomweko.