Numbers 20:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ameneŵa ndiwo madzi a ku Meriba kumene Aisraele adakangana ndi Chauta, ndipo Chauta adadziwonetsa pakati pa anthuwo kuti ndi woyera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Awa ndi madzi a Meriba; popeza ana a Israele anatsutsana ndi Yehova, ndipo anapatulidwa mwa iwowa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Awa anali madzi a ku Meriba, kumene Aisraeli anakangana ndi Yehova ndiponso kumene Yehovayo anadzionetsa yekha kuti ndi Woyera pakati pawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Awa ndi madzi a Meriba; popeza ana a Israyeli anatsutsana ndi Yehova, ndipo anapatulidwa mwa iwowa.