Numbers 20:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mutilole tsono tidzere m'dziko mwanu. Sitidzera m'minda mwanu kapena m'mipesa mwanu. Ndipo sitidzamwa madzi a m'zitsime zanu. Tidzangodzera mu mseu wanu waukuluwo basi, mpaka titadutsa dziko lanu.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tipitetu pakati pa dziko lanu; sitidzapitira pamunda, kapena munda wampesa, sitidzamwa madzi a m'zitsime; tidzatsata mseu wachifumu; sitidzapatukira kulamanja kapena kulamanzere, mpaka titapitirira malire anu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chonde mutilole tidutse mʼdziko lanu. Sitidzera mʼminda yanu kapena mu mpesa wanu, kapenanso kumwa madzi mʼchitsime chilichonse. Tidzayenda kutsata msewu waukulu wa mfumu ndipo sitidzapatukira ku dzanja lamanja kapena lamanzere mpaka titadutsa malire a dziko lanu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tipitetu pakati pa dziko lanu; sitidzapitira pamunda, kapena munda wampesa, sitidzamwa madzi a m'zitsime; tidzatsata mseu wacifumu; sitidzapatukira kulamanja kapena kulamanzere, mpaka titapitirira malire anu.