Numbers 20:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Aroni saloŵa nao m'dziko limene ndidapatsa Aisraele. Adzafa, chifukwa choti nonse aŵirinu simudamvere lamulo langa ku madzi a ku Meriba kuja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Aroni adzaitanidwa kunka kwa anthu a mtundu wake; pakuti sadzalowa m'dziko limene ndapatsa ana a Israele, popeza munapikisana ndi mau anga ku madzi a Meriba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Aaroni adzakakhala ndi anthu a mtundu wake, sadzalowa mʼdziko limene ndapereka kwa Aisraeli, chifukwa nonse munandiwukira motsutsana ndi malamulo anga ku madzi a ku Meriba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Aroni adzaitanidwa kumka kwa anthu a mtundu wace; pakuti sadzalowa m'dziko limene ndapatsa ana a Israyeli, popeza munapikisana ndi mau anga ku madzi a Meriba.