Numbers 20:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo chifukwa chiyani mudatitulutsa m'dziko la Ejipito ndi kutifikitsa ku malo oipa ano? Kuno sikumera tirigu kapena mitengo ya mikuyu, kapena mitengo ya mipesa, kapenanso mitengo ya makangaza, ndipo kulibe ndi madzi akumwa omwe.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo munatikwezeranji kutitulutsa m'Ejipito, kutilowetsa m'malo oipa ano? Si malo a mbeu awa, kapena mkuyu, kapena mpesa kapena makangaza; ngakhale madzi akumwa palibe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chiyani unatitulutsa mʼdziko la Igupto ndi kutibweretsa kumalo woyipa ano? Kuno kulibe tirigu kapena nkhuyu, mphesa kapena makangadza. Ndipo kuno kulibenso madzi akumwa!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo munatikwezeranji kutiturutsa m'Aigupto, kutilowetsa m'malo oipa ano? Si malo a mbeu awa, kapena mkuyu, kapena mpesa kapena makangaza; ngakhale madzi akumwa palibe.