Numbers 20:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Tenga ndodo, ndipo iwe ndi mbale wako Aroni musonkhanitse mpingo, tsono ulamule thanthwe kuti litulutse madzi, anthu akuwona. Motero udzaŵatulutsira madzi m'thanthwe anthuwo, ndipo udzamwetsa mpingo wonsewo ndi zoŵeta zao zomwe.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tenga ndodoyo, nusonkhanitse khamulo; iwe ndi Aroni mbale wako, munene ndi thanthwe pamaso pao, kuti liwapatse madzi; potero uwatulutsire madzi m'thanthwe, ndi kumwetsa khamu la anthu ndi zoweta zao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tenga ndodo, ndipo iwe ndi mʼbale wako Aaroni musonkhanitse anthu onse pamodzi. Uyankhule ndi thanthwe ilo iwo akuona ndipo lidzatulutsa madzi ake. Udzatulutsa madzi mʼthanthwe limeneli kuti anthu onse ndi ziweto zawo amwe.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tenga ndodoyo, nusonkhanitse khamulo; iwe ndi Aroni mbale wako, munene ndi thanthwe pamaso pao, kuti liwapatse madzi; potero uwaturutsire madzi m'thanthwe, ndi kumwetsa khamu la anthu ndi zoweta zao.