Numbers 21:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu Yachikanani ya ku Aradi imene inkakhala kumwera, itamva kuti Aisraele akubwera, kudzera njira ya ku Atarimu, idathira nkhondo Aisraelewo, nigwirako ena ukapolo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene Mkanani, mfumu ya Aradi, wokhala kumwera, anamva kuti Israele anadzera njira ya Atarimu, anathira nkhondo pa Israele, nagwira ena akhale ansinga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu ya Akanaani ya ku Aradi, imene inkakhala ku Negevi, itamva kuti Aisraeli akubwera kudzera msewu wopita ku Atarimu, inachita nkhondo ndi Aisraeli nigwira ena mwa iwo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene Mkanani, mfumu ya Aradi, wokhala kumwela, anamva kuti Israyeli anadzera njira ya azondi, anathira nkhondo pa Israyeli, nagwira ena akhale ansinga.