Numbers 21:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Sihoni sadalole kuti Aisraele adutse dziko lake. Adasonkhanitsa anthu ake onse pamodzi, napita kukamenyana nkhondo ndi Aisraele kuchipululu, ndipo adafika ku Yahazi, namenyana ndi Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Sihoni sanalole Israele apitire m'malire ake; koma Sihoni anamemeza anthu ake onse, nadzakomana naye Israele m'chipululu, nafika ku Yahazi, nathira nkhondo pa Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Sihoni sanalole kuti Aisraeli adutse mʼdziko mwake. Iye anasonkhanitsa pamodzi ankhondo ake onse kuti akamenyane ndi Aisraeli mʼchipululu. Atafika pa Yahazi anamenyana ndi Aisraeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Sihoni sanalola Israyeli apitire m'malire ace; koma Sihoni anamemeza anthu ace onse, nadzakomana naye Israyeli m'cipululu, nafika ku Jahazi, nathira nkhondo pa Israyeli.