Numbers 21:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Aisraele adamgonjetsa ndi lupanga, nalanda dziko lake kuyambira ku mtsinje wa Arinoni mpaka ku mtsinje wa Yaboki, kufikira m'malire a dziko la Aamori, chifukwa malirewo anali otchinjirizidwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Israele anamkantha ndi lupanga lakuthwa, nalanda dziko lake likhale laolao, kuyambira Arinoni kufikira Yaboki, kufikira ana a Amoni; popeza malire a ana a Amoni ndiwo olimba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Aisraeli anamupha ndi kulanda dziko lake kuchokera ku Arinoni mpaka ku Yaboki, kulekezera mʼmalire a dziko la Aamoni, chifukwa malire a dziko la Aamoni anali otetezedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Israyeli anamkantha ndi lupanga lakuthwa, nalanda dziko lace likhale lao lao, kuyambira Arinoni kufikira Yaboki, kufikira ana ai Amoni; popeza malire a ana a Amoni ndiwo olimba.