Numbers 21:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Hesiboni unali mzinda wa Sihoni mfumu ya Aamori, amene adaamenyana ndi mfumu yakale ya Amowabu, ndipo adamlanda dziko lake lonse mpaka ku mtsinje wa Arinoni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Popeza Hesiboni ndiwo mudzi wa Sihoni mfumu ya Aamori, imene idathira nkhondo pa mfumu idafayo ya Mowabu, nilanda dziko lake m'dzanja lake kufikira Arinoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Hesiboni unali mzinda wa Sihoni mfumu ya Aamori, yemwe anamenyana ndi mfumu yakale ya dziko la Mowabu. Lonselo linakhala dziko lake mpaka ku Arinoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Popeza Hesiboni ndiwo mudzi wa Sihoni mfumu ya Aamori, imene idathira nkhondo pa mfumu idafayo ya Moabu, nilanda dziko lace m'dzanja lace kufikira Arinoni.