Numbers 21:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Moto udabuka ku Hesiboni. Malaŵi a moto adatuluka mu mzinda wa Sihoni. Moto udaononga Ari mzinda wa ku Mowabu, udapserezeratu mapiri a kumtunda kwa Arinoni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Popeza moto unatuluka m'Hesiboni, chirangali cha moto m'mudzi wa Sihoni; chatha Ari wa Mowabu, eni misanje ya Arinoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Moto unabuka ku Hesiboni, malawi a moto kuchokera mu mzinda wa Sihoni. Unanyeketsa Ari mzinda wa ku Mowabu, nzika za ku malo okwera a Arinoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Popeza moto unaturuka m'Hesiboni, Cirangali ca mota m'mudzi wa Sihoni; Catha Ari wa Moabu, Eni misanje ya Arinoni.