Numbers 21:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adamvera mau a Aisraelewo naŵaperekadi Akanani aja m'manja mwao. Aisraele adaŵaonongeratu Akananiwo pamodzi ndi mizinda yao yomwe. Choncho malowo adaŵatcha kuti Horoma.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anamvera mau a Israele, napereka Akanani; ndipo anawaononga konse ndi midzi yao yomwe; natcha dzina lake la malowo Horoma.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anamva pempho la Aisraeli ndipo anapereka Akanaaniwo kwa iwo. Anawawononga pamodzi ndi mizinda yawo. Kotero malowo anatchedwa Horima.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anamvera mau a Israyeli, napereka Akanani; ndipo anawaononga konse ndi midzi yao yomwe; nacha dzina lace la malowo Horima.