Numbers 21:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho zidzukulu zao zidatha nkufa, kuyambira ku Hesiboni mpaka ku Diboni, ndipo tidaŵaononga mpaka ku Nofa, pafupi ndi Medeba.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tinawagwetsa; Hesiboni waonongeka kufikira ku Diboni, ndipo tinawapululutsa kufikira ku Nofa. Ndiwo wakufikira ku Medeba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Koma ife tawagonjetsa; Hesiboni wawonongedwa mʼnjira monse mpaka kufika ku Diboni. Tawaphwasula mpaka ku mzinda wa Nofa, mzinda womwe umafika ku Medeba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tinawagwetsa; Hesiboni waonongeka kufikira ku Diboni, Ndipo tinawapululutsa kufikira ku Nofa, Ndiwo wakufikira ku Medeba.