Numbers 21:32 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mose adatuma anthu kuti akazonde Yazere. Ndipo Aisraele adagwira midzi yake, napirikitsa Aamori amene anali kumeneko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mose anatumiza anthu akazonde Yazere, nalanda milaga yake, napirikitsa Aamori a komweko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mose atatumiza azondi ku Yazeri, Aisraeliwo analanda midzi yozungulira ndi kuthamangitsa Aamori omwe ankakhala kumeneko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mose anatumiza anthu akazonde Yazere, nalanda miraga yace, napitikitsa Aamori a komweko.