Numbers 21:33 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adabwerera, nadzera njira ya ku Basani. Ogi mfumu ya ku Basaniko adatuluka kukalimbana nawo. Iyeyo pamodzi ndi anthu ake onse adakamenyana nawo nkhondo ku Ederei.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anatembenuka nakwera kudzera njira ya ku Basani; ndipo Ogi mfumu ya ku Basani anatuluka kukumana nao, iye ndi anthu ake onse, kudzachita nao nkhondo ku Ederei.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka anabwerera, nadzera njira ya ku Basani. Choncho Ogi mfumu ya ku Basani ndi gulu lake lonse lankhondo anatuluka kukakumana nawo ndipo anamenyana nawo ku Ederi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anatembenuka nakwera kudzera njira ya ku Basanu; ndipo Ogi mfumu ya ku Basana anaturuka kukumana nao, iye ndi anthu ace onse, kudzacita nao nkhondo ku Edreyi.